Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Bambo wazaka 70 akhala kundende zaka 14 chifukwa chogwililira

Bwalo lamilandu ku Balaka lalamula a Phutheya Galeta azaka 70 kuti akagwire ndende yakalavula gaga kwa zaka 14 chifukwa chochita zadama ndi mwana.

Ofalitsa nkhani za Polisi ya Balaka Gladson M’bumpha watsimikiza nkhaniyi ndipo wati a Galeta adagwilira mwanayo yemwe ndi wazaka 14 mwezi wa June,2024.

Oweluza milandu Joshua Nkhono wati wapereka chilangocho kuti ena atengerepo phunziro.

A Galeta amachokela mmudzi wa Malula kwa mfumu yaikulu Sawali ku Balaka.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Achewa athira nsembe

MBC Online

Lingadzi Police arrests hacker

Romeo Umali

‘Zitukuko zikufalikira ponseponse’

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.