Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

‘Tithandizane potukula ntchito za umoyo’

Akuluakulu ogwira ntchito za umoyo ku ofesi ya Mangochi apempha magulu akufuna kwabwino kuti agwire ntchito limodzi ndi ofesiyi pothandiza kupititsa patsogolo ntchito zaumoyo pakati pa anthu omwe akulandira thandizo la chipatala.

Pempholi ladza pamene gulu la apolisi lotchedwa Mangochi Women Police Network  lapereka thandizo losiyanasiyana kuphatikizapo chakudya kuchipinda cha ana operewera zakudya nthupi komanso chipinda cha anthu odwala chifuwa chachikulu.

Malingana ndi wapampando wa Mangochi Women Police Network, Sub Inspector Suzan Msongole, thandizoli ndi limodzi mwa ntchito zachifundo zomwe apolisiwa amagwira pofikira anthu omwe ndi ovutika.

Wina mwa katunduyu ndi sopo, mafuta ophikira shuga komanso ufa.

 

Olemba Owen Mavula

Related posts

Amumanga atanamiza anthu kuti amachulukitsa ndalama m’matsenga

Rabson Kondowe

Sports is a tool to transform the youths — Inkosana Nkosi

Romeo Umali

Chakwera to visit flood victims in KK, KA

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.