Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani

‘Akabaza alembetse njinga zawo’ 

Bungwe la Malawi Coalition of Kabaza Stakeholders Association (MACOKASA) lapempha ochita kabaza wa njinga zamoto kuti agwiritse ntchito mwayi omwe boma lapereka kuti alembetse njinga zawo pamtengo otsika. 

Bungweli lati kuyambira pa 24 July chaka chino lidzigwira ntchito yolimbikitsa a kabaza wa njinga zamoto kuti adzikalembetsa njinga zawo ku nthambi yowona za malamulo apa nsewu ndipo adziletsa anjinga zamoto omwe njinga zawo ndi zosalembetsa kulowa m’ma tawuni.

Wapampando wa bungwe la MACOKASA, a Moses Mwalabu, ati ntchitoyi ichitika m’madera osiyanasiyana a m’dziko muno, ndipo bungwe lawo lidzigwira ntchito ndi boma pofuna kulimbikitsa akabaza kukalembetsa njinga zawo komanso kuti adzikhala ndi zodziyenereza kuyenda pa nsewu monga zipewa zodzitetezera ziwiri pa njinga iliyonse.

Mmodzi mwa akuluakulu ku nthambi yowona za malamulo apamsewu, a Leonard Ntonya, ati pakadali pano nthambiyi yalowetsa m’kawundula njinga zamoto zoposa 12,000 kuyambira m’mwezi wa February chaka chino.

Iwo anadandaula kuti anthu omwe ali ndi njinga zamoto sakuyikapo chidwi chokwanira, ngakhale ichi chili chiyambi chabe.

Mkulu wa bungwe la Road Safety Alert Foundation, a Joel Jere, apempha aMalawi kuti adziwonetsetsa kuti akugwiritsa ntchito kabaza wa njinga zamoto zomwe ndi zolembetsa komanso zomwe zili ndi zipewa zodzitetezera pofuna kusamala moyo wawo komanso kupititsa patsogolo chitetezo m’dziko muno.

Boma lidapereka mwayi kwa akabaza kuti adzitha kulembetsa njinga zing’onozing’ono pa mtengo wa K56,000 ndipo zikuluzikulu pa mtengo wa K77,000.

Kudzera muzokambirana ndi bungwe la MACOKASA, boma lidawonjezera nthawi yomwe lidapereka kwa akabazawa kuchoka pa 30 June chaka chino kufika pa 30 December.

Olemba: Gracious Banda

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Plant trees with care — CASA

MBC Online

Ndatula pansi udindo wa utsogoleri wa aphungu otsutsa boma — Nankhumwa

MBC Online

Malawi’s Temwa Chawinga crowned world’s leading goal scorer of 2023

Alinafe Mlamba
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.