Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Osagulitsa ndi kugula chiponde – Unduna wazaumoyo

Unduna wazaumoyo wachenjeza anthu kuti asiye mchitidwe ogulitsa ndi kugula chiponde kapena kuti “Ready to Use Therapeutic Food” mu chingerezi.

Malinga ndi chikalata chomwe undunawu watulusa ndipo wasainira ndi mlembi wamkulu muundunawu, a Samson Mdolo, mchitidwewu ukukolezera kusowa kwa chiponde muzipatala zaboma.

Azaumoyo amapereka chiponde maka kwa anthu omwe ali onyetchera.

A Mdolo ati mchitidwewu ukuchitika ngakhale pamapaketi a chipondechi analemba kuti sichogulitsa, ndipo izi zithanso kudzetsa mavuto ena kwa anthu omwe akumadya opanda uphungu wa akatswiri azachipatala.

Pamenepa, iwo amemeza anthu m’dziko muno kuti adzikaneneza kupolisi anthu omwe akugulisa chiponde mosatsata malamulo.

Related posts

Ma Drone awaulutsa

Romeo Umali

Mayi amangidwa atamenya mwana wake mwankhanza ndikumutsira chitedze

Alinafe Mlamba

A Chakwera acheza ndi ochita malonda kunyumba ya boma

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.