Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Ophunzira amenya aphunzitsi powaganizira kuti akuchita za matsenga

Apolisi ku Chikwawa akufunafuna ophunzira omwe aphwanya ofesi ya mphunzitsi wamkulu pasukulu ya pulaimale ya Mitondo m’bomalo ati poganiza kuti mphunzitsi wamkuluyo akuchita zinthu za matsenga.

Wachiwiri kwa ofalitsankhani wapolisi ku Chikwawa, Chance Mfune, wati pa 29 November, ophunzira ena pasukulupo anakomoka kaamba kakuti kunatentha kwambiri.

Koma ophunzira ena anakwiya ndi izi ndipo anatengana kupita kunyumba kwa mphunzitsi wamkuluyo poganiza kuti ndi yemwe wachititsa izi kudzera mmatsenga.

Apa chipwirikiti chinabuka mpaka anawo anamenya aphunzitsi ena awiri komanso kuba chipangizo cha mphamvu ya magetsi a dzuwa (Solar Panel) cha pasukulupo.

Related posts

GOVERNMENT REDUCES THE PRICE OF PETROL

McDonald Chiwayula

Tigers claim bitter-sweet 3 points

Romeo Umali

DRAMA AT PAC MEETING

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.