Phwando la nyimbo la Ku Mingoli Bash likuyenera kupitilira opanda Onesimus potsatira pempho la oyimbayu kuti achotsedwe pamndandawu kaamba koti akonzi aphwandoli sanatsate dongosolo.
Akuluakulu omwe akuyendetsa phwandoli ati ndi odabwa komanso okhudzika ndi chiganizo cha Onesimus choti sakaimba nawo ku phwandoli.
Shadreck Kalukusha mkozi waphwandoli wati apeza mlowam’malo wa oyimbayi yemwe a Malawi adzakhutire naye.
Kudzera patsamba lake la mchezo, Onesimus wati palibe dongosolo lililonse la mgwirizano pakati pa iye ndi okonza phwando la nyimbo-li.
“Tawapempha kuti asiye kusochoretsa ndikunamiza anthu zoti ndikaimba kuphwandoli ndipo pakafunikira tipempha anzathu odziwa malamulo alowelerepo,” watero Onesimus.
Aka sikoyamba kuti oyimba asapezeke pa phwandoli. Chaka chatha oimba wamdziko la Jamaica, Alaine, anakanika kudzayimbanso kuphwandoli ndipo kumayambiliro achaka chino Young Stunna wamdziko la South Africa anamuchotsa pamndandawu kaamba koti amapezeka mmaphwando ochuluka anyimbo.