Bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF) latsimikiza kuti lipitiriza ntchito yothandiza anthu, kuphatikizapo amene anakhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi m’dziko muno.
Wapampando wa bungweli, a Jephta Mntema, amayankhula izi m’boma la Nkhotakota atathandiza mabanja omwe analipira inshulansi pa ngongole zawo okwana 21 mwa mabanja 3,000 ndi ndalama zokwana K25 million ngati chipepeso atakhudzidwa ndi ngozi ya kusefukira kwa madzi.
A Mntema analimbikitsanso anthu kuti adzipereka ndalama ya insulansi akamatenga ngongole zawo.
M’modzi mwa opindula, a Mccloud Jere, amene amakhala m’mudzi wa Mbuna m’bomali, ati akusimba lokoma atalandira ndalama zoposera K9 million kuchokera ku NEEF ngati chipepeso kaamba kakuti munda wawo wa mzimbe unakokoloka ndi madzi.
Olemba: Yamikani Makanga