Mphunzitsi wakale wa timu ya FOMO, Mapopa ‘Kent’ Msukwa, walangiza timuyi kuti isapusitsike ikasewera bwino ndi m’khala kale za timu ya pfuko lino ya Flames, yomwe ili pansi pa JK Legends Productions.
“Kunena ku mbali yoona m’mene angasewerere, siziwapatsa chithunzithunzi choona,” Msukwa watero.
Masewerowa akhalapo loweruka likubwerali pa bwalo la masewero la Mulanje ngati njira imodzi yotolera ndalama pamene a FOMO akukonzekera kuti asewere nawo mu mpikisano wa ligi yayikulu, imene iyambe mwezi wa April chaka chino.
Mwezi wathawu, timu ya FOMO idalowa mu ligi yayikulu itagonjetsa timu ya Ntopwa FC 4-3 pa mapenate mu mpikisano wa ligi ya kum’mwera ya Thumbs Up.