Nyumba youlutsa mawu ya boma, Malawi Broadcasting Corporation (MBC), yasayina mgwirizano ndi bungwe la Water Aid.
Cholinga cha mgwirizanowu ndi kupititsa patsogolo nkhani zokhudza ukhondo komanso kasamalidwe kamadzi.
Mkulu wa MBC, a George Kasakula, wati wayilesiyi ndiyodzipereka pofalitsa nkhani zachitukuko monga zamtunduwu ndipo alonjeza zokonza ma programme apamwamba okhudza madzi ndi ukhondo.
“Apa zili ngati kukankhira pumbwa kuchipwete chifukwa izi ndi zimene timapanga,” a Kasakula anatero.
Mkulu wa Water Aid m’dziko muno, a Peter Phiri, anayamikira mgwirizanowu ndipo anati akukhulupilira kuti uthandiza kukopa mabungwe ena othandiza pankhani zachuma , makamaka popititsa patsogolo nkhani zachitukuko chamadzi ndi ukhondo m’dziko muno.