Ndalama zokwana K327 billion ndi zomwe zapezeka, dziko lino litagulitsa fodya oposa ma Kilogramme 64 million pakutha pa sabata zisanu ndi ziwiri.
Ndalamazi ndi zochuluka kuyerekeza ndi momwe zidalili chaka chapitachi.
Ofalitsankhani wa bungwe la Tobacco Commission, Telephorus Chigwenembe, wati ndiwokondwa kuti mtengo ogulitsira fodya wakwera kuchoka pa $2.78 kufika pa $2.81, zomwe zabweretsa ndalama zokwana $182 million.

