Apolisi ku Lilongwe amanga Thokozani Charles wazaka 24 pomuganizira kuti anaba mafoni a mmanja awiri a ndalama pafupifupi K300,000 a mayi wina yemwe anamunamiza kudzera pamasamba a mchezo pa Facebook kuti amukwatira komanso ali ndi mankhwala othandiza kuti banja lawo lidakhale lolemera.
Mneneri wapolisi ku Lilongwe, Hastings Chigalu, wati Charles amagulitsa zovala za kaunjika pomwe mayiyo amakhalira ku Area 23 ku Lilongwe komweko. A Chigalu ati awiriwo anadziwana kudzera pa Facebook ndipo Charles anauza mkaziyo kuti agone naye ndicholinga choti mankhwala olemeretsawo agwire ntchito ndipo mkaziyo anavomera. Awiriwo anachita izi pamalo ena ogona alendo ku Area 50 ku Lilongwe komweko.
Usiku, kamberembereyo anauza mayiyo kuti apite pafupi ndi bwalo la zamasewero la Bingu kuti akachite zizimba zina. Ali komweko, Charles anauzanso mayiyo kuti akawaze zinthu zina zowoneka ngati zitsamba pa msewu wodutsa galimoto. Mmene zimachitika izi, mkaziyo anali atasiya mafoni ake a mmanja kwa njondayo.
Malinga ndi a Chigalu, apa Charles anapeza mpata ndikuthawa ndi mafoniwo.
Thokozani Charles ndi wa mmudzi wa Chitenje, mfumu yaikulu Kuntumanje ku Zomba.