Malawi Broadcasting Corporation
News

Kafukufuku akuti chikhulupiliro mwa aphungu ndi makhansala chikuchepa

Gawo loyamba la kafukufuku wa bungwe la Institute of Public Opinion and Research (IPOR) waonetsa kuti anthu ambiri akutaya chikhulupiliro ndi aphungu akunyumba ya malamulo ngakhalenso makhansala.

Kafukufukuyi ndi okhudza mmene aphungu akunyumba yamalamulo amagwirira ntchito ndipo anachitika kuyambira mwezi wa March chaka chino m’maboma ambiri kupatula boma la Likoma ndipo wapeza kuti pafupifupi anthu 44 pa 100 akuti aphunguwa sakwaniritsa malonjezo ndipo ndipo atatu pa 100 akutsimikiza kuti aphunguwa amakwaniritsa.

IPOR yapezanso kuti anthu ambiri akufuna kuti oyimira paudindo wa phungu adzikhala ndi digili, chimodzimodzinso ndi oyimira upulezidenti pomwe khansala adzikhala ndi diploma.

Mukafukuyi anthu ochuluka akuti akufuna kuti zochitika munyumba yamalamulo zidzikhala muchiyankhulo cha aMalawi kuti adzitha bwino kutsatira zochitika m’nyumbayi.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Students loans application surpass projections

MBC Online

MRCS yagawa K180 million m’boma la Karonga

MBC Online

‘Mavuto simathero a moyo’

Paul Mlowoka
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.