Eni kampani yopanga sopo ya Hirwa General Dealers ati agoma ndi mmene akugwilira ntchito kazembe wawo watsopano, Emmie Deebo.
Akuluakulu akampaniyi ati ntchito yomwe Emmie Deebo amayenera kugwira m’miyezi iwiri iye wayigwira mwezi umodzi, zimene zachititsa kuti kampaniyi ipange phindu lochuluka.
Atafunsidwa ngati awa ali magwiridwe ntchito oyenera, oyimbayu anati iye amakonda ndalama kotero akuyenera kugwira ntchito apeze ndalamayo.
Akuluakulu akampaniyi ayamikiranso unduna wazalonda poyika ndondomeko zokomera anthu kuchita malonda momasuka.