Bungwe la Chewa Heritage Malawi – Chifukwato cha a Chewa lauza a Enock Chihana kuti apepese mtundu wa a Chewa pazimene adayankhula pamsonkhano wa olembankhani Lachitatu munzinda wa Lilongwe.
Iwo ati a Chihana adayankhula mawu achipongwe pa msonkhanowo.
Wapampando wa bungweli, Mfumu Sosola, ati bungwe lawo lapereka masiku atatu kwa a Chihana kuti apepese kupanda kutero adzawaitana kuti akawaonetse kudambwe.