Awiri mwa anthu omwe alephera pa chisankho cha wachiwiri kwa mtsogoleri wachipani cha Malawi Congress (MCP) Engineer Vitumbiko Mumba komanso a Ken Zikhale Ng’oma ati iwo sagwa mphwayi koma kuthandiza chipanichi kuti chidzapambane pa chisankho cha chaka cha mawa.
Engineer Mumba wati agwira ntchito ndi Dr Chakwera komanso omwe apapambana, Mai Catherine Gotani Hara, polimbikitsa chipani cha MCP komanso kutukula dziko lino.
Nawo a Zikhale polankhakhula atagwirana paphewa ndi a Mumba komanso a Gotani Hara, anati iwo anabweranso kunsonkhanowu ngakhale alephera pofuna kuonetsa kuti sananyanyale koma akukondwera kuti wapambana ndi mzimayi, ndipo agwira limodzi ntchito.
Nawo a Gotani Hara auza MBC kuti akuthokoza Chauta komanso amuna awo powathangata kupambana, ndipo ati azifunsa nzeru ndi upangiri kuchokera kwa anthu omwe agonjawa kaamba ali ndi kuthekera kwina komwe iwo alibe.