Mkhalakale pa ndale yemwenso ndi m’modzi wa akuluakulu a chipani cholamula cha Malawi Congress (MCP) a Brown Mpinganjira apereka uthenga wachiyembekezo kwa anthu akudera la ku mmawa m’boma la Chiradzulu kudzera ku msonkhano omwe anachititsa mderali.
A Mpinganjira omwenso amadziwika ndi dzina loti BJ achititsa msonkhano pa bwalo la zamasewero la sukulu ya pulaimale ya Bandawe.
Mwa zina a Mpinganjira ati boma likuchita chirichonse chotheka pothana ndi mavuto omwe anthu akukumana nawo.
“Vuto lina lomwe anthuwa akukumana nalo ndi kusowa kwa chakudya,” anatero a Mpinganjira.
Pakadali pano a Mpinganjira ati boma lichita chotheka popereka chakudya komanso ndalama kudzera mu ndondomeko ya Mtukula Pakhomo kuti anthuwa akwanitse kugula zinthu zofunika.
Ena mwa atsogoleri omwe anali nawo pa msonkhanowu ndi wachiwiri kwa mkulu owona za achinyamata mchipani cha MCP a Blessings Chilembwe.
Olemba: Timothy Kateta