Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Muyembekezere ntchito zachitukuko zochuluka – Mia

Phungu wadera la Chikwawa Nkombezi, a Abida Mia yati aMalawi ayembekezere ntchito zachitukuko zochuluka pansi pa utsogoleri wa Dr. Lazarus Chakwera.

Phunguyi yemwenso ndi nduna yoona zamadzi ndi ukhondo yanena izi pa bwalo lasukulu ya sekondale yoyendera ya Nkumaniza m’bomali pomwe amachititsa msonkhano wachitukuko.

Pankhani ya ku dera lawo, iwo ati apitiriza kukonza misewu, kulimbikitsa ntchito zamaphunziro, zaukhondo komanso zachitetezo mderali.

Mmau ake, bwanankubwa wa boma la Chikwawa, a Nurdin Kamba wayamikira phunguyi  kuti ndi phungu amene amagwiritsa bwino ntchito ndalama za thumba lachitukuko la Constituency Development Fund (CDF).

A  Kamba atinso a Mia amayamba afunsa za zitukuko zomwe anthu ku dera lawo akufuna zomwe ati ndi chitsanzo chabwino pa nkhani yotumikira anthu.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

FARMERS URGED TO HARVEST RAINWATER

Rabson Kondowe

Chakwera to preside over Cyclone Freddy Memorial Service

Romeo Umali

Immigration appears before Parliament on passport printing saga

Aisha Amidu
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.