Olemba: Charles Wahara ndi McDonald Chiwayula
Mabungwe ndi mayiko omwe amathandiza dziko lino pa chitukuko atsindika kuti apitiriza kuthandiza ndondomeko ya chuma cha dziko lino chifukwa chakukhutitsidwa ndi njira zomwe boma lakhazikitsa pofuna kubwezeretsa chuma m’chimake.
Chitsimikizochi chaperekedwa pamsonkhano wokambirana za ndondomeko ya chuma cha dziko lino ya chaka cha 2026/2027, womwe unachitikira ku Bingu International Convention Centre muzinda wa Lilongwe.
Msonkhanowu unapereka mwayi kwa unduna wa zachuma kukambirana ndi mabungwe osiyanasiyana pa mfundo zofunika komanso njira zomwe zitsogolere ndondomeko ya chuma cha dziko lino ya chaka cha 2026/2027.
Poyankhula ndi MBC pamapeto pa msonkhanowu, a Mwanamvekha anati mabungwe othandiza akhutitsidwa ndi njira zomwe Boma lakhazikitsa pofuna kukonzanso chuma cha dziko lino.
“Ndizosangalatsa kuona kuti mabungwe othandiza akukhutitsidwa ndi njira zomwe takhazikitsa pothandiza kukweza chuma cha dziko lathu,” anatero a Mwanamvekha. “Zonse zomwe tikuchita ndi kukonzanso ndondomeko ndi ntchito za chuma kuti dziko lino lipite chitsogolo.”
Kazembe wa dziko la Germany ku Malawi, a Ute Konig anayamikira boma chifukwa cha kusintha ndi kukonza ntchito zachuma.
Iwo anati monga mabungwe othandiza, apitiriza kugwira ntchito limodzi ndi Boma m’magawo osiyanasiyana a ndondomeko ya chuma.
Unduna wa zachuma wakhala ukuchititsa misonkhano yosiyanasiyana yofuna kumva maganizo pa ndondomeko ya chuma cha dziko lino ya chaka chino kufika chaka cha mawa kuchokera kwa nzika za dziko lino ndi abwenzi a dziko lino pachitukuko.


