Mkulu oona zakachilombo ka HIV ndi matenda a edzi mu unduna wazaumoyo wati pakufunika kuika njira zoti zithandizire kukweza chiwerengero cha abambo opita kuchipatala kukayezetsa magazi komanso kulandira thandizo lachipatala loyenera ngati atapezeka ndi kachilombo kapena matenda a edzi.
A Rose Nyirenda ayankhula izi pamene bungwe la AIDS Healthcare Foundation (AHF) limakondwerera kuti lakwanitsa kuika anthu oposa 2 miliyoni omwe ali ndi matendawa pandondomeko yolandira thandizo lachipatala.
“Ngakhale tikuchita bwino polimbana ndi matendawa pali mavuto ena omwe tikuyenera kuthana monga kukweza chiwerengero cha ana komanso abambo olandira thandizo lachipatala,” atero a Nyirenda.
M’modzi mwa akulu akulu ku AHF, a Triza Hara, ati achilimika kugwira ntchito ndi boma powonetsetsa kuti anthu omwe ali ndi kachilombo ka HIV ali pandondomeko yamankhwala.
Malinga ndi unduna wazaumoyo, chiwerengero cha anthu amene ali pa ndondomeko yama ARV chadutsa 930,000.