Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News

‘Njanji itsitsa mitengo ya katundu’

Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wati akufunitsitsa kuti anthu adzigula katundu otsika ndipo wati izi ndi zotheka kudzera mu chitukuko cha njanji.

Iye wati chitukuko cha njanji chalimbikitsanso ubale ndi mgwirizano ndi mayiko ozungulira monga Mozambique ndi Zambia.

Dr Chakwera atinso akufunitsitsa kuti anthu adzikhala ndi chuma kudzera mundondomeko za boma, kuphatikizapo ngongole za NEEF, ndipo ati ndi masomphenya a chipani cha Malawi Congress (MCP) kuti idzale Njanji.

Iwo anapitilira kunena kuti zovuta zomwe zilipo boma likukonza ndipo zinthu zakhala bwino.

“Zitukuko zikupitilira ndipo ndizolimba,” anayankhula motero President Chakwera.

Dr. Chakwera wapemphanso anthu a m’boma la Nsanje kuti adzamuvotere komanso aphungu achipani cha MCP.

Pa msonkhanowu panalinso wachiwiri kwa mtsogoleri wa MCP m’chigawo cha kummwera, a Abida Mia, ndi akuluakulu ena a chipani MCP.

Olemba: Mercy Zamawa

Related posts

COMFWB empowers over 450 female entrepreneurs

Romeo Umali

Balaka Police launches manhunt for alleged reckless driver

Romeo Umali

Lions Club donates medical equipment to Chitipa Hospital

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.