Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Ochita bizinesi zing’onozing’ono apindula mu mgwirizano wa NBM ndi kampani zina

National Bank of Malawi (NBM) yasaina mgwirizano ndi kampani za Sky Energy Africa komanso 265 Energy.

Mu mgwirizanowu, makasitomala a NBM adzigula katundu wa kampani ziwirizi  kupyolera ku ngongole  yomwe adzigwirizana ndi bankyi.

Poyankhula atasainila mgwirizanowo, m’modzi mwa akuluakulu a bankiyi, a Oswin Kasunda, anati mgwirizanowu upinduliranso ochita bizinesi zing’onozing’ono zomwe zinalibe kuthekera kogula katundu wa kampani ziwirizi kaamba kakuchepekedwa nthumba.

A Kasunda atinso mgwirizanowo uthandizanso kuteteza zachilengedwe kaamba koti katundu wa kampanizi  amagwiritsa ntchito njira zambiri zachilengedwe monga dzuwa.

 

Olemba: Naomi Kamuyango

Related posts

Public Works Programme brings environmental assets to Mchinji

Romeo Umali

Military studies crucial in enhancing national security

MBC Online

Sendeza bemoans rising child abuse cases

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.