Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Apolisi amanga anthu 696

Apolisi amanga anthu okwana 696 omwe akuwaganizira kuti apalamula milandu yosiyanasiyana mdziko muno.

Malinga ndi mneneri wa  apolisi mdziko muno a Peter Kalaya, ntchitoyi aigwira masiku atatu kuyambira lachitatu sabata yatha.

A Kalaya atinso apeza katundu osiyanasiyana yemwe akumuganizira kuti ndiobedwa.

Katunduyu ndi monga galimoto ziwiri, zipangizo za magalimoto, mankhwala a mchipatala kudzanso zakudya zosavomerezeka ndi zina zambiri.

Malinga ndi a Kalaya, ntchitoyi yomwe aigwira ndi maiko monga Zimbabwe, South Africa, Zambia, Angola ndi ena,  zithandiza kulimbikitsa maubale a kagwiridwe ka ntchito kabwino kudzanso kukhwimitsa chitetezo mu Africa.

 

Olemba : Ghwabupi Mwabungulu

Related posts

Dr Usi ayamikira mpingo wa Anglican pothandizira boma pa chitukuko

Romeo Umali

Malawi weighs joining UN water conventions

MBC Online

Osewera mpira wa asungwana akusokonekera

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.