Malawi Broadcasting Corporation
Entertainment Local Local News Nkhani

10May wayamba kupepesa

Tendai ’10May’ Malata wayambapo kupepesa mayi Triephornia Thomson Mpinganjira, amene akuyenereka kuwapepesa kwa masiku atatu, malinga ndi chigamulo chabwalo la milandu.

Bwalo lamilandu ku Lilongwe Lolemba sabata ino linagamula kuti mkuluyu apepese mayiwa kwa masiku atatu atamupeza olakwa pa mlandu onyoza anthu ena pa makina a intaneti.

Oweruza anapereka chigamulo chakuti akakhale miyezi khumi kundende koma anayamba ayimitsa kaye chigamulochi kaamba kakuti aka kanali koyamba kuti a Malata apalamule.

Kutsatira kutero, adamulamula kuti apepese mayi Mpinganjira pogwiritsa ntchito njira yomwenso anawanyozera kwa masiku atatu motsatizana.

Malinga ndi malamulo, mulandu onyoza ena pa intaneti umatha kukhala kundende kapena kupereka chindapusa chosachepera K1 milion.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Titsegula misewu-yi pofika December chaka chino — Hara

Beatrice Mwape

Chakwera courts investors in rail sector

MBC Online

Dr Chakwera to attend late Reverend Mgawi’s funeral

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.