Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Yemwe anali wa polisi ku Zambia akakhala ku ndende chifukwa chakuba

Khothi mu mzinda wa Lilongwe lalamula Chimuka Muchimba wazaka 29 yemwe anali wapolisi mdziko la Zambia kukakhala ku ndende zaka 15 chifukwa chobera mzika ya dziko la China ndalama zokwana K20 million.

Mneneri wapolisi ku chigawo cha pakati ku zambwe, Foster Benjamin wati Muchimba anapalamula mlanduwu ndi mzake wa kuno ku Malawi Kelvin Mlenga wazaka 42 ochokera m’boma la Thyolo yemwenso walandira chigamulo chofanana.

Benjamin wati Muchimba pamodzi ndi mzakeyo anawopseza mzikayo ndi mfuti ya mtundu wa pistol komanso zikwanje kunyumba kwake kwa Njewa ku Lilongwe.

Apolisi anagwira awiriwo ku malire a dziko la Malawi ndi Zambia ku Mwami. Malinga ndi a Benjamin, Muchimba ankagwira ntchito yapolisi ndipo kwao ndi ku Zambia koma anamuchotsa ntchitoyo chifukwa chaumbava.

 

Olemba Charles Pensulo

 

Related posts

MPONDA NDI MPHUNZITSI WA SILVER STRIKERS

Romeo Umali

Band yanyimbo zauzimu yadziko lonse ibwera poyera

Rabson Kondowe

Tsogolo la mlandu wa a Mbedza lioneka masana ano

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.