President wa dziko lino yemwenso ayimire chipani cha Malawi Congress, Dr Lazarus Chakwera, watsimikizira anthu m’boma la Ntcheu kuti boma limaliza kupaka phula msewu wa pakati pa Tsangano ndi Neno.
President Chakwera wanena zimenezi pa sitolo zapa Kambilonjo, kuzambwe kwa boma la Ntcheu.
Dr Chakwera wati ndalama za msewuwo zilipo kale ndipo akudziwa kuti msewu wamakono udzathandiza pa ntchito za malonda ndi ulimi.
Iwo anati ndi okondwa kuti anthu m’boma la Ntcheu apindula ndi ngongole ya NEEF, komwe NEEF yapereka K2.1 billion.
Dr Chakwera watsimikizira anthu omwe sanapeze mwayi wa ngongolezo kuti NEEF ipitiriza kupereka ngongole.
Pa nkhani ya migodi, Dr Chakwera anati dziko lino linadalitsika ndi miyala ya mtengo wapatali ndipo ayetsetsa kuti chuma chochoka kumigodi chipindulire aMalawi kudzera ku thumba la Sovereign Fund.
President Chakwera pamenepa anapempha anthuwo kuti adzamuvotere pa chisankho chikudzachi.
Dr Chakwera tsopano akupita kwa Champiti mdera lakumvuma m’boma la Ntcheu.
Olemba: Isaac Jali


