Oyimba nyimbo za uzimu, Favoured Martha, wapereka thandizo la yunifomu kwa ana 23 ovutika apa sukulu ya pulaimale ya Chilobwe ku Blantyre.
Katswiriyu analimbikitsanso oyimba anzake kuti akhale ndi mtima othandiza ana amene ali ndi zosowekera kuti athe kupitiriza maphunziro awo.
Mphunzitsi wa mkulu pa sukuluyi, a Lucy Matemba, anati ndi okondwa kwambiri poti thandizoli labwera mu nthawi yake chifukwa ana ena amalephera kupita ku sukulu chifukwa chosowa yunifomu.
Olemba: Juliana Mlungama