Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani Politics

Anthu aku Ntchisi adzavotera Dr Chakwera

Anthu a kummwera kwa boma la Ntchisi atsindika kuti voti yawo adzapereka kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera komanso phungu waderali, a Ulemu Chilapondwa.

Polankhula pa msonkhano omwe unakozedwa ndi a Chilapondwa pabwalo la zamasewero la Sibawo, a Yobu Chikho, ochokera m’mudzi mwa Mavwanje, m’bomali, anatsimikiza kuti iwo ndi anzawo adzavotera Dr Chakwera chifukwa cha chitukuko chochuluka chomwe boma lake lachita m’dziko muno komanso m’boma la Ntchisi.

“Dr Lazarus Chakwera ndi mtsogoleri wamasomphenya. Ife alimi a kuno ku Ntchisi tikusangalala kwambiri chifukwa cha zomwe boma lake likutipangira monga fetereza wotsika mtengo komanso ngongole ya zipangizo za ulimi,” anatero a Chikho.

A Dickson Falison, omwe ndi a m’mudzi mwa Khuwi m’bomali, anafotokozanso kuti voti yawo ndi ya Dr Chakwera chifukwa cha momwe utsogoleri wawo wasinthira miyoyo ya anthu kudzera mu ntchito zosiyanasiyana zachitukuko m’dziko muno.

“Pano ku Ntchisi kwamangidwa zipatala, magetsi afika madera ambiri, madzi afikanso madera ochuluka. Komanso ife alimi tinalandira ngongole za NEEF zomwe zatithandiza kwambiri pa ulimi wathu chaka chino. Kotero palibe chifukwa chosinthira boma,” iwo anatero.

Khansala wadera la Mphunju, a Flackson Sefasi, anatsindikanso zomwezi ndi kuonjezerapo kuti boma la Dr Chakwera lidamanga mlatho wa Chikwatu ndi Chikuwi komanso misewu yosiyanasiyana.

“Ngati pali nthawi yomwe anthu akuno awona kusintha komanso kusangalala ndi nthawi yomwe boma la Dr Lazarus Chakwera lakhala likulamulira. Kuno anthu ankakusala, koma anangobwera a Chakwera pano zinthu zambiri
zikutifika ndithu ndiye Ife kuno voti yathu ndi ya Chakwera basi,” a Sefasi anatero.

Olemba: Mike Kalumbi

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Elderly man jailed for indecent assault

Romeo Umali

WOCACA FOR COLABORATION IN CANCER FIGHT

MBC Online

Ntchito yofufuza ndege m’dziko la Russia yayamba

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.