Malawi Broadcasting Corporation
Business Development Local Local News Nkhani

Chakwera akatsegulira chionetsero cha Trade Fair

Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera akuyembekezeka kufika ku Chichiri Trade Fair Grounds komwe atsegulire chionetsero cha za malonda.

Bungwe la Malawi Confederation of Chambers of Commerce and Industry (MCCCI) ndi lomwe likuchititsa chionetserochi, chomwe chikutsindika pa mfundo zolimbikitsa kupanga katundu woyenera kutumiza kunja kwa dziko lino.

Padakali pano, khamu la anthu lafika kale ku Chichiri komwe kuli kampani pafupifupi 177 zomwe zichite nawo zionetserozi kuyambira lero mpakana sabata yamawa, Lachitatu, pa 29 May.

Olemba: Earlene Chimoyo ndi Austin Kachipeya

 

Related posts

Usi ali ku mapemphero

Secret Segula

Namibia set for state funeral of President Geingob

McDonald Chiwayula

Mlandu wa a Bushiri ukupitilira lero

Alinafe Mlamba
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.