Zokonzekera za mwambo wa mapemphero okumbukira kuti dziko lino latha zaka 60 likudzilamulira omwe uchitike loweruka pa 6 July zili mchimake.
MBC inayendera malo omwe kuchitikire mwambo wamapempherowu ku Bingu International Convention Centre ndipo inapeza anthu omwe akugwira ntchito akumalizitsa zonse.
Wapampando wa komiti yokonzekera mapempherowa yemwenso ndi nduna yaza chitetezo a Harry Mkandawire ati cholinga chinali kukondwelera tsikuli mwa mphamvu m’madera onse a mdziko muno koma chifukwa cha imfa ya yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino malemu Dr Saulos Chilima ndi ena asanu ndi atatu, mtsogoleri wa dziko lino analamula kuti dziko lino likumbukire tsikuli pokhala ndi mapemphero.
Ndunayi yati dziko lino lakumana ndi mavuto ambiri ndipo likufunika machiritso.
Iwo apempha a Malawi kuti agwirizane mu nyengoyi ndi kuchita nawo mapempherowa.
Dziko la Malawi linalandira ufulu wodzilamulira mchaka cha 1964.