Apolisi kwa Jenda m’boma la Mzimba amanga a Robert Boma a zaka 34 atawapeza ndi chamba cholemera ma kilo 32 pamene amafuna kuti akwere nacho basi yopita ku Lilongwe.
Ofalitsankhani ku polisi ya Jenda, a MacFarlen Mseteka, akuti akwanitsa kugwira mkuluyu pambuyo potsinidwa khutu kuti a Boma anali ku Luwawa.
Apolisi atathamangirako, a Boma anathawira mu basi yomwe inali pa depoti.
Atawapeza, anawafufuza ndipo anawapeza ndi Chambacho chomwe sanatulutse msonkho wake, ndipo apolisi sanachedwetse koma kuwamanga kuti akayankhe mlandu.
A Boma ndi a m’mudzi wa Chiphazi kwa mfumu yayikulu Kasumbu m’boma la Dedza.