Nduna yoona chitetezo cha m’dziko, a Ken Zikhale Ng’oma, yati ziphaso zolowera ndi kutulukira m’dziko muno (ma passport) zikhala zikutuluka posachedwapa.
A Zikhale Ng’oma ati izi zili chomwechi chifukwa ntchito yosindikiza ma passport inayamba ndipo akuyesetsa kuti idzifulumira.
Iwo amatsimikizira anthu amene anapita ku ofesi za Immigration mu mzinda wa Blantyre, pamene iwo anakayendera malowa.
Pa tsiku, Immigration ikutulutsa ma passport okwana 500, omwe a Ng’oma ati ndi osakwanira.
Olemba: Charles Chindongo
#MBCDigital
#Video