Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Osagwiritsa ntchito imfa ya Chilima pa ndale

Chipani cha Malawi Congress (MCP) chati anthu ayenera kulemekeza mzimu wa yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino malemu Dr.Saulos Chilima posauseweretsa pa nkhani za ndale.

Mlembi wamkulu wa MCP, a Richard Chimwendo Banda amayankhula pa bwalo la za masewero la Baka m’boma la Karonga pa msonkhano omwe anachititsa ndi wachiwiri woyamba kwa mtsogoleri wa chipanichi, a Catherine Gotani Hara.

Mmawu awo, a Gotani Hara omwenso ndi Sipika wa nyumba ya malamulo anati boma la Dr Lazarus Chakwera likugawa zitukuko mosayang’ana dera.

Wapampando wa MCP mchigawochi, Kezzie Msukwa anayamikira anthu a m’boma la Karonga kaamba kokonda chipani cha MCP.

Pa mwambowu panalinso aphungu a chipani cha DPP, a Mungasurwa Mwambande a Karonga north komanso a Werani Chilenga a m’boma la Chitipa.

 

Olemba Grant Mhango

Related posts

Chakwera arrives in Blantyre

Rabson Kondowe

Makolo asiya mwana pa golosale

Blessings Kanache

New vehicle fleet to improve MBC’s service delivery

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.