Nduna ya za malonda a Vitumbiko Mumba yachenjeza kuti boma sililekelera kuti aMalawi avutike ndi kukwera kwa mitengo ya zinthu kaamba ka anthu ena adyera.
A Mumba, omwenso adzayime ndi mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera pa 16 September pano, ayankhula izi m’boma la Mzimba pa misonkhano yoyimayima.
Iwo anati boma lili tchelu kuthana ndi wina aliyense yemwe akukwezera dala mitengo ya katundu pofuna kupweteka aMalawi.
Izi zikutsatira malipoti a kupezeka kwa sugar komanso cement zomwe anati anthu ena osakonda dziko lawo amabisira dala, zomwe boma la Dr Chakwera likuthana nazo.
Olemba: Grant Mhango



