Adindo amene akumanga Matambo Substation m’dziko la Mozambique ati aMalawi ayembekezere kupitilira kukhala ndi magetsi odalilika pamene ntchito yogula magetsi m’dzikolo ikuyembekezeka kuyamba pofika mwezi wa May chaka chamawa.
Magetsi a Matambo Substation azifika pa Phombeya Substation m’dziko muno.
Engineer wamkulu pa Matambo Substation ku Tete a Suraj Prakash wawuza olembankhani a m’dziko muno amene anakayendera ntchitoyi kuti amaliza ntchitoyi pofika mwezi wa December chaka chino ndipo ntchito yomanga njira yodutsamo magetsiwa itha mwezi wa May usanafike.
Ntchitoyi ikuyembekezera kuwonjezera magetsi a nkhaninkhani zomwe zipangitse kuti magetsi apitilire kusazimazima.
Olemba: Justin Mkweu, Tete, Mozambique


