Bungwe la NEEF lati liri mkati mokonza ndondomeko zoti likhale likugawa ngongole ya zaulimi wa mthirira kuyambira mwezi wa April chaka chino.
Mkulu wa bungweli, a Humphrey Mdyetseni, ati posachedwapa akhala akufikira alimi a m’maboma onse m’dziko muno omwe akhale m’magulu osachepera makumi asanu ndi kuwapatsa ngongoleyi.
Cholinga chake ndi kuti alimi adzilima mbewu zosiyanasiyana pogwiritsa ntchito madzi a m’madambo ndi mitsinje.
Izi akuti zidzathandiziranso powonetsetsa kuti dziko lino liri ndi chakudya chokwanira nthawi zonse.
A Mdyetseni anapitirizanso kunena kuti ndondomeko idzakhala ikupitirira kufikira nyengo ya zaulimi odalira mvula.
Pakadali pano, a Mdyetseni atsindika zakufunika koti alangizi apitirize kutenga nawo gawo lalikulu lophunzitsa alimi onse njira komanso ndondomeko zamakono zaulimi ndi cholinga chakuti adzikwanitsa kulima mbewu zawo zomwe angamagulitse ndi kukwaniritsa kubwenza ngongole zomwe atenga.