Malawi Broadcasting Corporation
Business News Nkhani

Mlingo wa kukwera mtengo kwa zinthu (inflation) watsika mu February

Mlingo wa kukwera mtengo kwa zinthu (inflation rate) watsika mu February chaka chino kufika pa 33.5 percent kuchoka pa 35 percent mu January.

Izi ndi malinga ndi nthambi ya National Statistical Office (NSO).

Kutsikaku ndi kaamba ka kutsika kwa mlingo wa kukwera mtengo kwa zakudya m’dziko muno.

Mlingo wa kukwera mtengo kwa zakudya watsika kufika pa 42 percent mu February kuchoka pa 44.9 percent mu January.

Banki yayikulu ya Reserve inakweza mlingo wa chiongoladzanja chomwe mabanki amalipira akakongola ndalama ku bankiyi (policy rate) kufika pa 26 percent ndicholinga choti mlingo wakukwera mtengo kwa zinthu (inflation rate) uyambe kutsika.

Related posts

Ridley College students extend helping hand to Jacaranda

Alinafe Mlamba

Chiganizo chotuluka mu mgwirizano tidzatsimikiza pa 19 July — UTM

Romeo Umali

Chakwera for co-existence, rallies youths on development

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.