Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wati pa sitolo zapa Lizulu pakufunika town yabwino, chipatala chachikulu komanso ofesi yayikulu ya apolisi pofuna kulimbikitsa chitetezo.
Dr Chakwera walimbikitsa bata ndi mtendere pa nyengo ino yokopa anthu ndipo anapempha achinyamata kuti asamalore kutumidwa ndi anthu andale kuti adziyambitsa zipolowe.
Iwo anati boma likuganizira zokuza Lizulu kukhala tauni yamakono kaamba koti ndi msika otchuka kwambiri m’dziko muno komanso pochitikira malonda pakati pa aMalawi ndi anthu aku Mozambique.
Pa nkhani ya zokolola, Dr Chakwera ati posachedwapa boma lipeza njira yothandiza kuti pakhale makina opangira katundu osiyanasiyana kuchoka ku mbewu monga tomato, kachewere ndi zina kaamba kakuti nthawi zina zinthu zimenezi zimangowonongeka.
Pamenepa, Dr Lazarus Chakwera analangiza anthu kuti adzatuluke mwaunyinji kukaponya voti la 16 September pano.
Olemba: Isaac Jali


