Bungwe la Malawi Chewa Heritage lapereka zipangizo zomangira nyumba ya mfumu yayikulu Ngabu m’boma la Nsanje.
Nyumba ya mfumuyi idaoonongeka ndi mphepo yamkhutho imene idawomba dera la Khuluvi m’mudzi wa Kaudzu.
Mtsogoleri wa bungwe la Chifukato Cha Achewa, Gogo Sosola, anati ndi kofunika kukhala mothandizana komanso modalirana panthawi yamavuto.
“Apapa tangoyamba ndipo tidzibwera bwera maka munthawi yamavuto komanso chisangalaro kuti tiyende limodzi ngati dziko,” Gogo Sosola anatero.
Mfumu yayikulu Ngabu anali okondwa polandira thandizoli.
“Ndine othokoza kwambiri pa zimene mwatipatsazi, ine ngati mfumu ndi makhala ku nyumba ya ufumu koma banja langa liri ndi pogwira,” iwo anatero.
Pamwambowu panali anthu osiyanasiya kuchokera ku boma, ochita malonda komanso mafumu, ndi ena ambiri.
Katundu amene anaperekedwa ndi monga malata komanso cement ndi ndalama.
Olemba: Stanley Kadzuwa