Malawi Broadcasting Corporation
Agriculture Local Local News Nkhani

‘Banja likuyembekezera kupeza K650 million pansi pa Mega Farm’

A Agness Nkhoma, omwe akuchita ulimi pamodzi ndi amunawo kwa Mkanda m’boma la Mchinji, ati akuyembekezera kupeza ndalama zoposera K650 million kuchokera ku chimanga chomwe analima pa mahekitala 240 pansi ndondomeko ya Mega Farms.

Iwo ayankhula izi pomwe wachiwiri kwa nduna ya zaulimi, a Benedicto Chambo, amayendera ena mwa alimi omwe analandira zipangizo za ulimi pa ngongole pansi pa ndondomeko ya Mega Farms, yomwe cholinga chake mkufuna kulimbikitsa alimi kulima mbewu pa minda yayikulu kuti adzipeza phindu lochuluka.

A Nkhoma, omwe anapuma pa ntchito atagwira kwa zaka zochuluka ngati mlangizi wa zaulimi, athokoza boma kaamba ka ndondomeko ya Mega Farms, yomwe ikumapereka zipangizo za ulimi kwa alimi pa ngongole, mwa zina.

Mega Farms Unit, yomwe ndi imodzi mwa nthambi mu unduna wa zaulimi, ikuyembekezera chimanga choposera matani 200,000 kwa alimi 855 omwe anachita nawo mgwirizano olima chimanga chogulitsa ku Admarc komanso National Food Reserve Agency (NFRA).

A Chambo ati boma liyesetsa kupereka ndalama zokwanira ku ADMARC ndi NFRA kuti akwanitse kugula chimangachi, ochita malonda (mavenda) asanayambe kuwagula alimi pa mtengo wosavimelezeka.

Iwo alimbikitsa ogwira ntchito m’boma komanso achinyamata kuti akhale pa tsogolo kuchita ulimi ngati bizinesi kuti atukuke pa chuma.

Mkulu wa Mega Farms Unit, a Henry Msatilomo, wati alimiwa akuyenera kugulitsa mbewu zawo ku ADMARC komanso NRFA, kotero ati akuyembekezera kuti mabungwe awiriwa apeza ndalama zokwanira kuti agule chimanga chonse kwa alimiwa.

Iwo ati chaka chino alimi achita bwino kuyerekeza ndi chaka chatha, ngakhale kuti panali mavuto ena ndipo ati zimenezi zikapitilira, vuto lakuchepa kwa chakudya m’dziko muno, likhoza kukhala mbiri yakale.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Bankers sign Kansungwi

Romeo Umali

ILO CALLS FOR ACCELERATION OF ANTI-CHILD LABOUR EFFORTS

MBC Online

Ligi ipitilira mwezi ukaooneka — Classic U-20 Volleyball

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.