Senior Chief Mpando yakwa Kambilonjo ku Ntcheu, yayamika boma chifukwa chopereka ngongole yokwana K2.1 billion kwa anthu m’bomali kudzera ku NEEF.
Pomulandira President Chakwera, Senior Chief Mpando yati ngongole zimenezi zalimbikitsa ulimi kaamba koti anthu akulima katatu pachaka tsopano.
Mfumuyi yati anthu akugula mbewu komanso ma pump ochitira ulimi wanthilira.
Komabe mfumuyi yapempha boma kuti limalize kupaka phula msewu wa pakati pa Tsangano ndi Neno omwe wadutsa mderalo.
Iwo apemphanso boma kuti likonze ndondomeko yothandiza kuti anthu adzipindula ku ntchito za mgodi omwe uli mderalo.
Yemwe ayimire chipani cha MCP ngati phungu wadera la Dzonzi Mvai, a Mwayi Kamuyambeni, apempha madzi abwino, chakudya komanso mlatho pa mtsinje wa Thava omwe umalumikiza anthu a mdera la Kambilonjo ndi Phalula m’boma la Balaka.
Olemba: Isaac Jali


