Bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF) lalimbikitsa alimi m’dziko muno kuti adzichitanso ulimi wa ziweto pambali pochita ulimi wa mbewu zosiyanasiyana.
Mkulu wa bungweli, a Humphrey Mdyetseni, anena izi ku Msinja m’boma la Lilongwe komanso mdera la Mfumu yayikulu Chilikumwendo m’boma la Dedza komwe amapereka ngongole ya zipangizo zaulimi ndi kuyendera alimi omwe abzala kale mbewu zawo atalandira ngongoleyi.
A Mdyetseni ati pambali polima mbewu zosiyanasiyana, alimiwa akhozanso kumaweta ziweto ndi kumakagulitsa ku mayiko ena, zimene akuti zikhoza kuthandizira kuti dziko lino lidzipeza ndalama zakunja.
Iwo anaonjezera kuti NEEF ndi yodzipereka popereka ngongole ya ziweto komanso yazipangizo za ulimi kwa alimi omwe ali m”magulu ngati alimiwo aonetsa chidwi.
A Madalitso Siliva, omwe ndi wapampando wa Sikimu ya Kachowe mdera la Mfumu yayikulu Masula m’boma la Lilongwe ndipo alandira ngongole ya K36 million, ati akonzeka kubzala mbewu zambiri pofuna kuthana ndi vuto la njala komanso kuthana ndi umphawi.
Mfumu yayikulu Chilikumwendo ya m’boma la Dedza yayamikira bungwe la NEEF kaamba kopereka ngongole ya zipangizo zaulimi mdera lawo.
Mfumuyi yapempha bungweli kuti lipereke ngongole ya zipangizo zaulimi nthawi yabwino ndi cholinga choti alimiwa adzikonzekeranso nthawi yabwino pomwe akuyembekeza kuyamba ulimi wa nyengo ya mvula.


