Mkulu wa kampani ya NACALA Logistics, a Chandra Mahon Singh, ati kuyambira sabata ya mawa adzikwanitsa kubweretsa malita a mafuta okwanira 2 million ndipo ati ali ndikuthekera konyamula mafuta pafupifupi malita 4 million pa ulendo umodzi.
Pakadali pano, a Singh ati kampaniyi idzinyamula mafutawa pakamodzi pa ulendo wa masiku awiri kuchokera ku Nacara kufika ku Lilongwe.
Iwo ati ntchito yokonza njanji ya Kanengo kupita ku Balaka yatha ndipo apitiriza kukonzanso njanjiyi pakati pa Kanengo ndi Mchinji kukafika ku Zambia ndipo ntchitoyi itha m’mwezi wa October.
Iwo ati kmpani yawo ndiyodzipereka kuthandiza boma pa ntchito za mtengatenga, makamaka ponyamula katundu osiyanasiyana.