Bus ya FCB Nyasa Big Bullets sinabwerere kuma ofesi atimuyi, dzulo italandidwa ndi ma Sherrif.
Bus-yi inalandidwa kaamba koti timuyi inali ndi ngongole ya ndalama zokwana K25 million ndi mphunzitsi wawo wakale Franco Ndawa.
Malingana ndi modzi mwa akuluakulu a Bullets, a Albert Chigoga, timuyi yalipira ndalamayi kuphatikizapo K4 million ndipo akudikira ndondomeko zokhudza malamulo kuti bus-yi ibwerere zomwe akuyendetsa ndi owayimira pamilandu.
Chigoga watsutsaso kuti timuyi ili ndi malingaliro ochotsa osewera ena pazifukwa kuti akupangila dala kuti timuyi isamachite bwino.
Lachiwiri, osewera a Bullets anakana kuchita zokonzekera za timuyi.
By Praise Majawa