Malawi Broadcasting Corporation
Agriculture Local Local News Nkhani

Boma lati alimi atha kukolora zochuluka

Alimi m’boma la Neno ati ali ndi chikhulupiliro kuti ayamba kukolora zochuluka kutsatira upangiri wamakono omwe apeza kudzera mmaphunziro awulimi.

Unduna wa za ulimi, kudzera mu ndondomeko ya Malawi Watershed Services Improvement Project (MWASIP), ndiumene unachititsa maphunzirowa.

M’modzi wa alimiwa, a Masautso Pagone, ochokera mmudzi mwa Kalupsa anena izi pa mwambo opereka masatifiketi kwa ophunzira 85 atachita maphunziro aulimiwa kwa chaka.

Mwazina, alimiwa aphunzira mmene angapangire manyowa, kubzyala mitengo yobwenzeretsa chonde, kukaphunzitsa anzawo komanso kuchita mabizinesi an’gonoang’ono ndi ndalama zimene amalandira zachitikuko za ‘Tisamale Chilengedwe’.

Mkulu owona zamapologamu ku dera loona za ulimi m’boma la Blantyre, a Annly Msukwa, ati ndi zokondweretsa kuti alimiwa awasula kuti akakhalenso zitsanzo komanso aphunzitse mmadera awo kuti boma la Neno lichite bwimo pa ulimi.

A Msukwa atinso maphunzirowa athandiza kubwenzeretsa zachilengedwe ndi nthaka kaamba kakuti bomali ndi limodzi mwa maboma omwe nthaka inaguga komanso zachilengedwe zikuwonongeka.

Malinga ndi wachiwiri kwa mkulu owona ntchito za MWASIP, a Joseph Kanyangalazi, mwa maboma asanu ndi awiri komwe bungweli ;ikugwirako ntchito, alimi a m’boma la Neno agwiritsa bwino ntchito komanso kupindula ndi ndalama za thumba la Tisamale Chilengedwe.

A Kanyangalazi ati izi zili chomwechi chifukwa alimiwa amachita mabizinesi ndi kupititsa patsogolo miyoyo yawo.

Kuyambira m’chaka cha 2021 alimi 1,165 aphunzira ulimi wamakono kudzera ku MWASIP.

Olemba: Beatrice Juma

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

“A Gotani – Hara ali ndi luntha potsogolera” — President Chakwera

Timothy Kateta

MPONDA NDI MPHUNZITSI WA SILVER STRIKERS

MBC Online

SHIRE VALLEY TRANSFORMATION PROGRAMME PHASE 2 GETS A BOOST

McDonald Chiwayula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.