Ngati gawo limodzi lokumbukira tsiku la mwana wa mu Africa, bungwe la Plan International mogwirizana ndi mabungwe ena, ati ana m’dziko muno akufunika thandizo lalikulu losiyanasiyana kuti akule bwino.
Akuluakulu oona za ana anati ndi kofunika kwambiri kuonetsetsa kuti ana akulandira thandizo loyenerera.
Wapampando wakomiti yoyang’anira ana ku Mzimba North, a Mthemzemu Kamanga, anati ngakhale pali zovuta zotere zinthu zikuyenda bwinobe m’chigawo chakumpoto.
“Ndikaona momwe ana monga ongoyendayenda m’misewu akuvutitsira mchigawo chakummwera ndi pakati, ndikuona kuti bolako kuno,” anatero a Mthezemu.
Chisangalalo cha tsiku la mwana wa mu Africa chifika pachimake lachinayi pa 24 July pamwambo omwe utachitikire pabwalo la Thumbi kwa Mfumu Yaikulu Jalavikuwa ku Mzimba.
Olemba: Henry Haukeya


