Malawi Broadcasting Corporation
Business Development Local Local News Nkhani

Mlimi apata mphoto ya K10 million

A Lyson Jickson, amene ndi mlimi wa m’boma la Lilongwe, apambana mphotho yaikulu ya K10 million ya mpikisano wa khisimisi omwe kampani ya lamya za m’manja ya TNM idaakonza kuyambira m’mwezi wa December chaka chatha.

A Jickson apata mphothoyi pa maere omaliza amene anachitikira mu mzinda wa Blantyre lachinayi.

Polankhula kudzera pa lamya, mkuluyu, amene poyamba amayakha mokayika atamva za nkhaniyi poyesa kuti mwina ndi akuba, anati ndalamayi iwathandiza pa ntchito yawo ya ulimi.

Winanso yemwe wapeza mphotho yaikulu ya K1 million ndi katswiri oyimba nyimbo za chamba cha Reggae yemwe amatsogolera gulu la Black Missionaries, Anjiru Fumulani.

Mkulu owona za malonda ku TNM, a Madalitso Jonazi, wati ndi okondwa kuti kudzera mu mpikisanowu, akwanitsa kupereka mphotho kwa makasitomala awo 2741 ndipo agwiritsa ntchito ndalama zoposa K62 million.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Top performing teachers awarded

Yamikani Simutowe

Tobacco sales resume at Kanengo

MBC Online

Habitat for Humanity advocates Disaster-Resilient construction

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.