Malawi yagonja 2-0 ndi Tunisia pa bwalo la masewero la Stade Olympique Hammadi Agebri munzinda wa Tunis. Awa anali masewero a mpira wamiyendo odzigulira malo mumpikisano wa 2026 World Cup.
Zigoli za Tunisia adamwetsa ndi Seifeddine Jaziri pamphindi 86 ndi Elias Achouri pamphindi 90+2 kudzera pa penote. Osewera wa Malawi, Lloyd Aarod, adapatsidwa Red Card mu mphindi 64.
Mwayi wa Flames unapezeka pa mphindi 90+8 kudzera pa penate koma ikakuona litsiro siikata, goloboyi wa Tunisia, Aymen Dahmen, anakwanitsa kuuchotsa penateyo imene anamenya Richard Mbulu.
Zateremu mu gulu H ndiye kuti Flames ili pa nambala 6 ndi ma point 6, pamene Tunisia ikutsogolera gululi ndi ma point 16.