Malawi Broadcasting Corporation
Business Development Local News Nkhani

Titukuka tikakonza misonkho, magetsi — Old Mutual

Mkulu wa kampani ya Old Mutual m’dziko muno, a Edith Jiya, ati dziko lino likuyenereka kuti likonze mavuto a magetsi komanso misonkho pofuna kuti dzikoli litukuke kudzera mu ndondomeko ya ATM.

Ndondomekoyi anakhazikitsa ndi mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera, mu mwezi wa February, ndipo cholinga chake ndi kukweza chuma cha dziko lino pogwiritsa ntchito ulimi, zokopa alendo komanso migodi.

A Jiya amayankhula izi pa mwambo wa akuluakulu a kampane zambiri m’boma la Mangochi komwe anati mfundozi zitha kutukula dziko la Malawi mwa ka nthawi kochepa.

Uthenga wawo pa mwambowu, iwo anati anthu akufunika kuti adziwe zakufunika kopanga katundu woti azigwiritsidwa ntchito m’dziko muno m’malo moyitanitsa kunja kwa dziko lino.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

COURT ADJOURNS MUSSA CONVICTION REVIEW CASE

MBC Online

Mangochi records 267 cases of pink eye disease

MBC Online

RBM OPTIMISTIC OF CONTAINING INFLATION

Justin Mkweu
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.