Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Tisagwire ntchito monyinyilika -Chakwera

Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wati anthu ogwira ntchito m’boma asamagwire ntchito monyinyilika chifukwa zotsatira zogwira ntchito mosadzipereka amavutika ndi aMalawi.

Mtsogoleriyu wati boma lake silisekelera mchitidwe wachipwilikiti komanso kugwira ntchito mosalumikizana ndi maofesi ena.

Dr Chakwera ati sukulu ya MSG ithandiza anthu ogwira ntchito m’boma kuti pogwira ntchito yawo adziika dziko lawo patsogolo.

Mtsogoleriyu walamula kuti Mlembi wamkulu muofesi mwao agwire ntchito ndi alembi a maunduna osiyanasiyana komanso atsogoleri a kampani za boma kuti adzitumiza ogwira ntchito ku sukuluyi kuti aphunzitsidwe bwino zantchito yawo.Tsopano sukuluyi yatsegulidwa kuti itumikire anthu onse m’dziko muno komanso ena ochokera m’maiko a kunja.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Ufa othandizira ovutika ndi njala wafika

Blessings Kanache

THYOLO – MAKWASA ROAD CUT OFF

MBC Online

Malawi improves on World Press Freedom Index ranking

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.