Malawi Broadcasting Corporation
Local News

Tipitiliza kulumikizitsa anthu omwe anathawa kwawo – MRCS

Bungwe la Malawi Red Cross Society (MRCS) lati lipitiriza ntchito yake yolumikizitsa nzika zomwe zinathawa kwawo zomwe zikukhala pa msasa wa Dzaleka kuti zidzilumikizana komanso kukumana ndi abale awo.

Mlembi wamkulu ku bungweli a Chifundo Kalulu ayakhula izi pa msasa wa Dzaleka pomwe bungweli limaunikila nzika zomwe zinathawa kwawozi momwe zingatsatire ndondomeko zothandizira  kulumikizana ndi abale awo mwaulere.

Iwo ati kuchokera pomwe bungweli linakhazikitsa ndondomekoyi mchaka cha 2012, bungwe la Malawi Red Cross lakwanitsa kulumikizitsa anthu ambiri ndi abale awo.

M’modzi mwa akuluakulu ku nthambi ya boma yoona za anthu omwe anathawa kwawo a Amos Mkandawire ayamikira bungwe la Malawi Red Cross pokhazikitsa ndondomekoyi ponena kuti ithandizira ana amasiye omwe ali pa msasawu kuti athe kulumikizana ndi abale awo ku maiko a kwawo.

 

Olemba: Madalitso Mhango

Related posts

Balaka Police to promote road safety, strengthen security over Easter

Romeo Umali

There was overuse of antibiotics during COVID — WHO report

Romeo Umali

TNM Super League mid-season Analysis

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.